You are on page 1of 16

VOL. 5 NO.

18 3 16 SEPTEMBER 2014
Kukwaniritsa ufulu wolankhula zakukhosi
MA ARV ABOWOKA KU
THYOLO NDI MULANJE
C
H
I
T
H
U
N
Z
I

:
N
A
T
I
O
N

L
I
B
R
A
R
Y
Ma ARV ndi mankhwala odula kwambiri
P
amene boma
likusinkhasinkha momwe
lingapezere mankhwala
okwanira pofuna kuteteza
miyoyo ya omwe adapezeka ndi
kachilombo ka HIV, kafukufuku
wathu wapeza kuti ogwira ntchito
mzipatala ku Thyolo ndi Mulanje
akugulitsa ma ARV kwa alimi ndi
ophika mowa.
Alimi akugwiritsa ntchito
mankhwalawa podyetsa ziweto
kuti zikule ndi kunenepa msanga
ncholinga choti azigulitse
pamtengo wokwera pamene
otcheza kachasu ndi mtonjane
amafuna ma ARV kuti mowa
wawo ukhale waukali kwambiri.
Mtolankhaniyu adayendera
maboma awiriwa sabata lathali
komwe adatsimikiza kuti
mankhwalawa akugulitsidwa
mwakathithi.
Mlimi wina mmudzi wa
Katundu mdera la Mfumu
Chimaliro ku Thyolo, a Maxwell
Hapala, adati amagula mankhwala
wa pamtengo wa K25 mbulu
umodzi ndipo botolo la mibulu 30
likugulitsidwa K750.
Koma ngati muli nawo ndipo
mukufuna kugulitsa pamtengo
wokwelerapo, titha kukambirana.
Nkhumba zanga sizikukula
msanga. Ndiye ndikufuna ndipeze
ma ARV kuti ndikasakanize ndi
deya kuti zikule msanga komanso
zinenepe, adatero Hapala.
Koma alimi ndi ophika mowa
ammudzi wa Kamoto adati anali
atangogula kumene mankhwalawa
kwa mlangizi wa za umoyo, a Justin
Chikopa, moti sakanatha kugula
ena mtolankhaniyu adatawauza
kuti ali ndi ma ARV ogulitsa.
A Chikopa anali atapita ku
chinkhoswe ku Makande pamene
mtolankhaniyu adafika kukhomo
kwawo, koma akazi awoa
Getrude Chikopaadatsimikiza
zoti amuna awo amagulitsa
mankhwala.
A Getrude Chikopa adati
amagulitsa botolo la mibulu 30
pamtengo wa K4 000.
Ndipo mtolankhaniyu
atadandaula kuti amuchotsere,
iwo adati mtengo wotsiriza ndi
K3 500 kaamba koti ndalamayi
amagawana amuna awo ndi
ogwira ntchito pachipatala cha
Chisoka omwe amawapatsa
mankhwala kuti azigulitsa.
Pabotolo lililonse, adokotala
amatengapo K2 000 pamene
WATIPASO MZUNGU JNR
Mutharika
wakana kukweza
malipiro a nduna
MTOLANKHANI WATHU
Pulezidenti Peter Mutharika
wakana kukweza malipiro a
nduna za boma lake.
Malingana ndi chikalata
chomwe mlembi wamkulu
wa boma, a Willie Samute,
anatumiza kwa a Mutharika pa
Ogasiti 20 2014 chikusonyeza
kuti nduna zikufuna malipiro
awo a pa mwezi akwere kuchoka
pa K600 000 ndi kufika pa K3.5
miliyoni kaamba ka kukwera kwa
mitengo ya zinthu.
Malipirowa akuphatikiza
chilichonse chomwe ndunazi
zimalandira monga ndalama
zogula mayunitsi a foni, mafuta
a galimoto, phoso la paulendo,
zolipirira nyumba zawo zogona
ndi zinthu zina.
Poyankhapo pa nkhaniyi a
Mutharika anati: Malipiro
a nduna sakwera kapena
kusintha.
Pulezidentiyu sanafotokoze
chifukwa chomwe wakanira
kukweza malipirowo, koma mkulu
wa bungwe loona za ufulu wa
ogula la Consumers Association
of Malawi (Cama), a John Kapito,
anati boma silingakweze malipiro
anduna popeza lili mmavuto a za
chuma.n
amuna anga amadyapo K1 500,
iwo adatero.
Titawayimbira, mkulu
woyanganira zaumoyo mboma
la Thyolo, a Dr. Michael Murowa,
komanso mlembi wamkulu mu
unduna wa zaumoyo, a Dr. Chris
Kangombe, adati sakudziwa
kanthu pa za nkhaniyi.
Nkhaniyi idatulidwa mmanja
mwa polisi ya Mikolongwe ndipo
mkulu wapolisiyi, Assistant
Superintendent Macoffman
Yamungo, wauza FUKO kuti
apolisi omwe adakachita
chipikisheni kunyumba kwa
a Chikopa adapeza mabotolo
enanso 6 zomwe zidachititsa
kuti banja limeneli limangidwe
nthawi yomweyo.
Ndipo titalitengera kubwalo
lamilandu ku Midima, a Getrude
Chikopa adavomereza kulakwa
kwawo. Apa khoti lidawalamula
kuti apereke chindapusa cha
ndalama zokwana K15 000
kapena kukaseweza jele kwa
miyezi 6, atero a Yamungo.
Koma iwo ati wogamula
milandu sadapereke chilango
chilichonse kwa a Justin Chikopa
kaamba kosowa umboni
wokwanira.
Moti panopa tikutolera
umboni kuti tikamumangalirenso
mkuluyu, iwo atero. n
3 16 SEPTEMBER 2014
2
Kukwaniritsa ufulu wolankhula zakukhosi
NDEMANGA
ZA MDZIKO
Nduna za nyika pa
nkhani ya malipiro
Nkhani yoti nduna zikufuna malipiro awo apa mwezi
akwere kuchoka pa K600 000 kukafika pa K3.5
miliyoni ndiyokhumudwitsa kaamba koti aliyense
akudziwa kuti dziko lino lili pa mavuto a za chuma.
Ndunazi zapereka pempholi nthawi yolakwika
kaamba koti boma likulephera kukonza bajeti
chifukwa choti lili ndi ngongole zambirimoti
zina likulephera kubwezakomanso mabungwe
ndi mayiko omwe amathandiza dziko lino anasiya
kupereka thandizo anthu ena ogwira ntchito mboma
ataba ndalama zoposa K13 biliyoni ku Lilongwe.
Iyi ndi nkhani yochititsa manyazi komanso
yomvetsa chisoni chifukwa ndalamazo zikanatha
kugula mankhwala mzipatala za boma, komanso
kugwira ntchito zosiyanasiyana za chitukuko.
Kuphatikiza apo, boma lili pampanipani chifukwa
choti linalonjeza zinthu zambiri nthawi ya
kampeni moti ndalama zomwe limapeza silingathe
kukwaniritsa malonjezanowo.
Ichi nchifukwa chake Amalawi ambiri akhumudwa
ndi pempho la ndunazo chifukwa choti aliyense
amayembekezera nduna kumvetsetsa mavuto omwe
boma likukumana nawo.
Apa zikuwonetseratu poyera kuti nduna zambiri
sizili pa mpando kufuna kutumikira Amalawi koma
zofuna zawo.
Tiyamikire Pulezidenti Peter Mutharika potemetsa
nkhwangwa pa mwala kuti sakweza malipiro
a ndunazo chifukwa dziko lino lili pa mavuto
adzawoneni a za chuma.
A Mutharika akhale tcheru ndi mchitidwe wa anthu
ena omwe amalowa ndale pofuna kudzitumikira
kapena kudzilemeretsa. n
M
abungwe a
A d v e n t i s t
De v e l o p me n t
and Relief Agency (Adra)
ndi a Water for All la ku
Sweden posachedwapa
apereka mijigo itatu kwa
anthu a mdera la Mfumu
Chikumbu mboma la
Mulanje ndi cholinga
chofuna kupititsa patsogolo
ntchito za chitukuko cha
madzi.
Mabungwewa achita izi
kaamba koti midzi yambiri
ya mderalo imasowa madzi
aukhondo.
Poyankhula pamwambo
wopereka mijigoyo, yemwe
anayimirira Water for All, a
Bo Wigren, anati bungwe
lawo ndi la Adra apereka
mijigoyo kwa anthu a
mmidzi ya Chinomba,
Kampala ndi Njoloma
omwe anati amakumana
ndi mavuto adzawoneni
osowa madzi.
A Wigren anati amayi
ndi ana amayenda mitunda
italiitali kukafunafuna
madzi aukhondo.
Mavutowa tsopano atha
ndipo amayi akhala ndi
nthawi yokwanira yogwira
ntchito za chitukuko, iwo
anatero.
Mfumu Chikumbu,
Werengani nyuzipepala ya FUKO
nthawi zonse. Iyi ndi nyuzipepala
yanuyanu ya ulere. Funsani kumene
imafikira mdera lanu kuti mudzilandira
nthawi zonse. Kapena lemberani kwa:
Circulation Manager
Nation Publications Limited
P. O. Box 30408
CHICHIRI, BLANTYRE 3.
Kukwaniritsa ufulu wolankhula zakukhosi
Mabungwe apereka mijigo
A Wigren akujiga pamene DC wa boma la Mulanje, a Jack Nguluwe,
akusamba mmanja
C
H
I
T
H
U
N
Z
I
:

S
A
M

M
A
J
A
M
A
N
D
A
BUYAZONKE
SAM MAJAMANDA
yomwe inali mlendo
w o l e m e k e z e k a
p a m w a m b o w o ,
inayamikira Adra ndi
Water for All chifukwa
chothandiza anthu a
mdera lake.
Iwo anapempha
mabungwewa kuti akumbe
mijigo ina mdera lake
popeza muli mavuto a
akulu akusowa kwa madzi
aukhondo.
Wachiwiri kwa mkulu
wa Adra, a Michael Usi,
analangiza anthu omwe
alandira mijigoyo kuti
ayisamale bwino ngati
imodzi mwa njira zosonyeza
kuthokoza kwawo.
Mijigoyo yadya
K9 miliyoni yomwe
yachokera ku Water for
All pamene Adra ndi
yomwe imayanganira
ntchito yokumba komanso
kuwonetsetsa kuti mijigoyo
yapitadi kwa anthu omwe
amayenera kuyilandira.
MANA
3 16 SEPTEMBER 2014 3
ZAULAMULIRO WABWINO
B
ungwe la za chisankho
la Malawi Electoral
Commission (MEC)
lichititsa zisankho pa
Okotobala 7 2014 mmadera
momwe mulibe aphungu ndi
mankhansala.
Dziko la Malawi linachititsa
zitsankho za aphungu pa
Meyi 20 koma kaamba ka
kupambana kwa a Peter
Mutharika kummawa kwa
boma la Thyolo komanso
kumwalira kwa mmodzi mwa
anthu omwe amapikisana
nawo pa pampando wa
phungu kumpoto kwa
Blantyre zisankho za aphungu
sizinachitike mmaderawa.
A Mutharika, womwe
anayima ngati phungu wa
mdera la kummawa kwa
Thyolo, anatula pansi mpando
wa uphungu atapambana ngati
pulezidenti wa dziko lino.
Pamene ku Thyolo ndi ku
Blantyre anthu akuvotera
aphungu, ku wodi ya Lisanjala
ku Machinga, Kandeu ku
Ntcheu, Lifupa ku Kasungu,
Mbalachanda ku Mzimba
Chisankho chapadera
chichitika pa Okutobala 7
ndi Zgeba ku Karonga anthu
akhala akuvotera makhansala.
Mneneli wa MEC, a
Sangwani Mwafulirwa,
anauza FUKO kuti bungwe
lawo ladzipereka kuti
zisankho zapaderazi zikhale
zapamwamba ndipo atulutsa
kale ndondomeko ya momwe
zinthu ziyendere.
C
H
I
T
H
U
N
Z
I
:

N
A
T
I
O
N

L
I
B
R
A
R
Y
RACHEL KACHALI
Mbendera: Achinyamata alembetse
WATIPASO MZUNGU JNR
Bwanamkubwa wa boma la
Chiradzulu, a James Manyetera,
achenjeza makhansala
ambomali kuti asalowetse
ndale pa ntchito za chitukuko
kuti bomali litukuke kwambiri
mzaka zisanu zikudzazi.
Polankhula Lachitatu
lathali pomwe ankatsegulira
msonkhano wa makhansala
ndi atsogoleri a mabungwe
akumidzi, a Manyetera
adatsindika kuti madera ambiri
mdziko muno akukanika
kupita patsogolo kaamba ka
mchitidwe wa andale ena
wolowetsa ndale pa chitukuko.
Makhansala asalowetse ndale pa chitukuko
Mwambowu udakonzedwa
ndi bungwe lolimbikitsa
ulamuliro wabwino la Pan
African Civic Educators
Network (Pacenet) ndi
thandizo la ndalama lochokera
ku Tilitonse.
Pacenet ikugwira ntchito
yolimbikitsa anthu akumidzi
kuti adzitengapo gawo pa
ntchito zachitukuko komanso
kupereka maganizo awo pa
zomwe zikuchitika mmadera
awo.
Koma a Manyetera
adatengerapo mwayi kulangiza
andale kuti asiyiretu mchitidwe
wolowetsa ndale pachitukuko
kuti dziko lino litukuke.
Iwo adati mchitidwe
wolowetsa ndale pa chitukuko
umachititsa kuti omwe
sakugwirizana ndi chipani
chomwe phungu kapena
khansala adayimira asatengepo
gawo pa zomwe zikuchitika
mmadera awo.
Tsono mkatero ndiye
kuti mukuphwanya ufulu wa
anthu pachitukuko monga
ikunenera ndime 30 ya
malamulo a dziko lino. Ntchito
ya khansala ndikuwonetsetsa
kuti masomphenya a
anthu akukwaniritsidwa
pachitukuko, adatero
bwanamkubwayu.
Mkulu wa Pacenet, a
WATIPASO MZUNGU JNR
Bungwe la At-Tariqatul Qadriah
Sunni Association (AQSA)
lachenjeza kuti pakhala povuta
kuti mafumu asiye mchitidwe
wa ziphuphu ngati boma
komanso mabungwe omwe
amalithandiza sakuwapatsa
chochita mafumuwa.
Mafumu ambiri
akudzudzulidwa chifukwa
chosalemekeza ufulu
wachibadidwe wa anthu
komanso kulanda malo a anthu
osauka potengera mphamvu
zomwe ali nazo.
Koma mkulu wa AQSA,
a Sheikh Fahad Zaidu
Muhammad, wachenjeza kuti
izi sizidzatha ngati palibe njira
zoyenera zothandizira mafumu
kupeza chuma pawokha.
Iwo adapereka chenjezoli
masiku apitawa pambuyo
popereka anapiye ankhuku
zanyama kwa mafumu 200
mboma la Balaka.
A Muhammad adati iwo
adaganiza zothandiza mafumu
ndi anapiye ngati njira imodzi
yowathandizira kupeza njira
zopezera ndalama pawokha kuti
asiye mchitidwe wa ziphuphu.
Iwo adati mafumu ambiri
alibe njira zopezera ndalama
ndipo ichi ndi chifukwa
amalowa mmayesero opempha
chipondamthengo pa ntchito
iliyonse yomwe angachitire
anthu awo.
Tikukhulupilira kuti anapiye
akakula adzawathandiza kupeza
ndalama ndi zina zofunikira
pakhomo pawo mosavutikira.
Tipemphenso boma ndi
mabungwe olithandiza kuti
alowererepo ngati tikufuna kuti
mafumu athu asiye ziphuphu,
adatsindika a Muhammad.
Iwo adati anapiye omwe
adagawa adali a ndalama
zokwana K14 miliyoni ndipo
adapatsidwa ngati mphatso
kuchokera kwa kampani ya
Central Poultry ku Lilongwe.
Nyakwawa Mtumbwe
idathokoza AQSA kaamba
ka thandizoli. Iyo idati
ikuyembekezera kudziyimira
payokha pachuma akayamba
kugulitsa nkhukuzi. n
Mafumu
akuchita
ziphuphu
kaamba ka
umphawi
Steven Duwa, adapempha
makhansalawa kuti athandize
poyendetsa zitukuko zomwe
zikulandira ndalama kuchokera
ku matumba a Constituency
Development Fund (CDF) ndi
Local Development Fund (LDF).
A Duwa adati iyi ndi njira
yokhayo yomwe ingathetse
mchitidwa wa ziphuphu
komanso kuwonetsetsa kuti
adindo akuchita zinthu poyera.
Pacenet ikugwira ntchito
yophunzitsa anthu za maufulu
komanso udindo wawo
pachitukuko mmaboma a
Chiradzulu, Machinga, Thyolo
komanso ku manisipalite ya
Luchenza.n
Ndondomeko ya
momwe zisankho ziyendere
ikhazikitsidwa pa Ogasiti 25.
Anthu oyendetsa zisankho
monga ma DC akhala
akufotokozera anthu momwe
zisankho ziyendere, anatero a
Mwafulirwa.
Mkulu wa MEC, a Maxon
Mbendera, anati kalembera wa
zisankhozi achitika kuyambira
pa Seputembala 4 mpaka 8.
Malo onse ochitira
kalembera azitsegulidwa
kuyambira 8 koloko
mmawa mpaka 4 koloko
madzulo. MEC idzakhalanso
ikulemba mkaundula wa
voti achinyamata amene
adzakwanitse zaka 18 pofika
pa 7 October, iwo anatero.
Abambo omwe apikisane
nawo pachisankho cha
phungu wa Nyumba ya
Malamulo adzapereka
K200 000 pamene amayi
adzapereka K150 000 pamene
abambo omwe apikisane nawo
pa ukhansala adzapereka K20
000 ndipo amayi K15 000.
Onse omwe akufuna
kudzapikisana nawo akuyenera
kupereka zikalata zawo ku MEC
pa Seputembala 9 2014. n
3 16 SEPTEMBER 2014
4 ZA AMAYI NDI JENDA
Wofad ikonza ndondomeko za ntchito
BRIGHT KUMWENDA
B
ungwe loona za
ufulu wa amayi la
Women for Fair
Development (Wofad)
likukonza ndondomeko
la mmene ligwirire
ntchito mzaka zisanu
zikudzazi.
P o l a n k h u l a
pamsonkhano womva
maganizo a anthu pa
chikonzerocho chomwe
chinachitika mu mzinda
wa Blantyre, mkulu wa
Wofad, a Linnah Matanya,
anati dongosololo
lipereka chikhulupiriro
mwa mabungwe omwe
amathandiza bungwe
lawo.
Bungwe la World
University Service of
Canada (WUSC) Malawi
ndi lomwe likuthandiza
Wofad kukonza
dongosololo lomwe
liyambe kugwiritsidwa
ntchito chaka cha 2015
mpaka cha 2020.
Mkulu wa WUSC
Malawi, a Jacob
Mapemba, anati bungwe
lawo linayamba kugwira
Z
I
T
H
U
N
Z
I
:

W
A
T
I
P
A
S
O

M
Z
U
N
G
U

J
N
R
C
H
I
T
H
U
N
Z
I
:

W
A
T
I
P
A
S
O

M
Z
U
N
G
U

J
N
R
Matanya: Ndife wokondwa
Zimba kulankhula pamsonkhanowo
powalera, iwo adatetero.
Iwo adatsindikanso
USaid ipempha mabanja achepetse
chiwerengero cha ana
WATIPASO MZUNGU JNR
Bungwe la United States
Agency for International
Development (USaid)
lati dziko la Malawi lili
pa chiopsezo chachikulu
pachuma ndi chitukuko
kaamba ka chiwerengero
chochuluka chomwe banja
limodzi limakhala nacho.
Polankhula pamwambo
wokumbukira kuchulaka
kwa anthu womwe
udachitira pabwalo la
Malundani mboma la
Machinga sabata lathali,
mkulu woyanganira za
moyo wa ana ku USaid,
a Evelyn Zimba, adati
kafukufuku akusonyeza
kuti mayi mmodzi
amakhala ndi ana 6.
A Zimba adati
c h i w e r e n g e r o c h i
nchachikulu kwambiri
poganizira chuma komanso
kuchuluka kwa malo
olimapo omwe mabanjawa
ali awo.
Choncho, ndikupempha
makolo omwe mudakali
kubereka kuti tiyeni
tichepetse chiwerengero
cha ana athu kuti
asadzasunduke chipsinjo
ntchito ndi Wofad
mchika cha 2012.
WUSC Malawi
ikufuna kuphunzira
Wofad dongosolo la
kagwiridwe ka ntchito
kuti azitha kupeza
thandizo kuchokera kwa
mabungwe a mdziko
muno komanso akunja,
anatero a Mapemba.
WUSC yakhala
ikuphunzitsa Wofad
kagwiritsidwe ndi
kuwerengera ndalama
zochokera kwa abwenzi
ake.
Ta p h u n z i t s a n s o
mamembala a
Wofad mmene
angachitire mabizinesi
osiyanasiyana, anatero
a Mapemba.
WUSC Malawi ndi
Wofad akugwiriranso
limodzi ntchito yopititsa
patsogolo ufulu wa amayi.
Ntchitoyo ikulandira
thandizo kuchokera ku
thumba la ndalama la
Tilitonse. n
kuti nthawi yakwano yoti
mabanja azibereka ana
Mapemba: Wofad ikuchita bwino
okhawo omwe akudziwa
atha kuwasamalira
mosavutikira.
A Zimba adatinso
nzachisoni kuti 25
peresenti ya achinyamata
a zaka zapakati pa 1525
adayamba kale kubereka
ngakhale kuti matupi awo
adakali anthete.
Iwo adati izi zikuchitika
chifukwa choti dziko
lino lilibe zipatala
zomwe zingathandize
achinyamata kupeza njira
zakulera.
Koma a Zimba
adathokoza bungwe la
Health Policy Project
(HPP) kaamba kochilimika
pa ntchito yozindikiritsa
anthu zakufunikira
kotenga njira zakulera
pofuna kuchepetsa
kuchulukana kwa anthu. n
3 16 SEPTEMBER 2014 5 ZA MAPHUNZIRO
B
ungwe la Evangelical
Association of
Malawi (EAM)
lalangiza mafumu ndi
atsogoleri amipingo a
mboma la Mulanje kuti
azitenga chitukuko ngati
utumiki womwe Mulungu
adawapatsa.
Mkulu wa pulojeketi ya
Tonse Tipindule, yomwe
imaphunzitsa anthu za
migodi, a Ruth Mwenda,
ndiwo analankhula
izi posachedwapa pa
msonkhano wophunzitsa
anthu za migodi mdera
la Mfumu Mabuka
mbomalo.
Cholinga cha
msonkhanowo chinali
kuphunzitsa anthu
zaubwino ndi kuyipa kwa
EAM iphunzitsa mafumu, abusa
SAM MAJAMANDA migodi komanso momwe
nzika ziyenera kupindulira
ku ntchito za migodizo.
A Mwenda adati
nthawi zambiri atsogoleri
azipembedzo amabwezera
mmbuyo nkhosa zawo
poziuza kuti zitukuko
ndi za dziko osati
zakumwamba.
Uku ndi kulakwa
chifukwa chitukuko ndi
udindo womwe Mulungu
adasiyira munthu padziko
lapansi atamulenga.
Tikawerenga mbuku
la Genesesi 1 tipeza
mawu womwe Mulungu
adawauza Adam ndi Eva
kuti asamalire dziko la
pansi ndi kuchita nalo;
zomwe zikusonyeza kuti
Mulunguyo sadana ndi
kutukuka kwa dziko la
pansi. Iye amafuna dzikolo
tilitukule moyenera
posamalira chilengedwe
chake, adatero a
Mwenda.
Iwo anadzudzulanso
mafumu ena omwe
anati amachititsa anthu
awo kuti asapindule ndi
ntchito za migodi zomwe
zikuchitika mmadera
mwawo pomalandira
ziphuphu kuchokera
kwa makampani okumba
miyala ya mtengo
wapatali.
Mafumu adyerawa
a m a l i m b i k i t s a
makampani a migodiwa
kuti aziwononga za
chilengedwe, anatero a
Mwenda.
Pothirirapo ndemanga
pa nkhaniyi, Mfumu
Fulama idayamikira EAM
pokumbutsa atsogoleri
zokhudza udindo wawo.
Ife anthu a ku
Mulanje tikuyembekezera
kupindula ndi ukadaulo
womwe talandira
panowu, iwo anatero.
Mwa zina, anthu
aphunzira momwe
angakambirane ndi
akuluakulu a migodi,
zomwe malamulo a dziko
lino amanena pa migodi
komanso zomwe anthu a
mdera omwe muli migodi
ayenera kuyembekezera
kuchokera ku makampani
okumba miyala.
EAM ikugwira
ntchitoyi mmaboma
a Mulanje, Mwanza
komanso Chikwawa ndipo
likuyembekezera kuti anthu
akumudzi azitengapo gawo
pomanga mfundo zokhudza
migodi.MANA
DZIWANI ZA MISONKHO
Nthambi ya boma yotolera msonkho ya Malawi
Revenue Authority (MRA) layamba kulipiritsa
chindapusa eni a galimoto zomwe zakhala masiku
oposera khumi (10) pa boda osawombola.
Izi zadza Kamba koti anthu ambiri amayitanitsa
galimoto ndikungozisiya pa boda. Malinga ndi
mkulu wa MRA, a Raphael Kamoto, galimoto
iliyonse yokhala pa boda kuposera masiku khumi
izalipiritsidwa K5,000 pa tsiku lina liri lonse
lowonjezera.
Anthu ambiri amangogula galimoto nkuzisiya
pa boda zomwe zimapangitsa kuti malo osungira
galimoto akhale osakwanira. A MRA amayeneranso
kuwonetsetsa kuti apereka chitetezo chokwanira
pa galimoto zomwe zimakhala mmaboda. Izi
zimawonongetsa ndalama chifukwa bungwe la
MRA ntchito yake ndikulipiritsa msonkho galimoto
zolowa osati kusunga galimotozo.
MRA ikudziwitsa anthu onse amene amayitanitsa
kapena akufuna kuyitanitsa galimoto kunja kwa
dziko lino kuti azikonzeka mokwanira (posunga
ndalama zowombolera) asanayitanitse galimoto
; izi zithandiza kuti galimoto zanu muthe
kuwombola mwachangu kutinso chindapusachi
chisakukhuzeni.
Ngati mukufuna kudziwa zambiri pa nkhaniyi;
pitani ku ofesi ina iliyonse ya MRA mdera lanu kuti
akakupatseni ndondomeko yoyenera poyitanitsa
galimoto yanu. Ndi udindo wanu kudziwa za
msonkho womwe mungalipire pa galimoto yomwe
mukufuna. n
Chindaputsa
posawombola
galimoto mu
nthawi yake
Ngati mufuna kudziwa zambiri, gwiritsani ntchito izi:
Tenifoni: 0888958220, 0999551634, 0888474644 kapena pa 01832685,
Fakisi: 01822 302, Email: tax@mra.mw
Keyala: Commissioner General, Malawi Revenue Authority, P/Bag 247, Bt.
WATIPASO MZUNGU JNR

Boma lati limanga sukulu
zitatu zophunzitsirako
maluso antchito zamanja
mboma la Machinga
pofuna kuchepetsa mavuto
omwe achinyamata
akukumana nawo kaamba
ka ulova.
Bwanamkubwa wa
bomali, a Reinghard
Chavula, adaulula
makonzero amenewa
pabwalo la zamasewero
la Malundani sabata
latha pazochitikachitika
zokumbukira kuchulakana
kwa anthu.
Bungwe la United States
Agency for International
Development (USaid) ndi
lomwe lidapereka thandizo
lochitira zochitika pofuna
kukumbutsa anthu za
kuyipa kobereka ana
mopyola muyezo.
Kafukufuku yemwe
mabungwe angapo
achita posachedwapa
akusonyeza kuti mayi
mmodzi amabereka ana
6 mdziko muno, zomwe
akuti zikuopseza chitukuko
cha dziko.
Ndipo polankhula
pamwambowu, a Chavula
adati kuchulukana
kwa anthu kwachititsa
kuti boma lilephere
kukwaniritsa ntchito
zotumikira anthu
pachuma, maphunziro,
umoyo ndi zina.
Iwo adapempha
mabanja omwe adakali
kubereka kuti achepetse
chiwerengero cha ana
awo molingana ndi chuma
chomwe iwo ali nacho.
Mayiwa adati mikangano
yomwe imakhalapo
nthawi yogawa makuponi
ndi umboni wokwanira
kuti anthu adachulukana
mopyola muyezo ndipo
boma likulephera kufikira
aliyense.
Boma lapeza kuti
chimodzi chomwe
chimachititsa anthu
kudalira boma pa
chilichonse ndi kusowa kwa
maluso antchito zamanja
pakati pa achinyamata.
Ndipo pofuna kuthana
ndi vutoli, boma limanga
sukulu zitatu zosulirako
achinyamata ndi maluso
antchito zamanja, a
Chavula adatero.
Nd i k u p e mp h a n i
achinyamata nonse amene
mudalekera sukulu yanu
panjira, kaya mudakwatiwa
ndi kukwatira, tiyeni
tikalembetse ku sukulu
zimenezi kuti tipeze
maluso osiyanasiyana
omwe adzatithandize
kudziyimira patokha, iwo
adapiritiza.
Mkulu woyanganira
zamoyo wa ana ku USaid,
Evelyn Zimba, adapempha
makolo kuti awonetsetse
kuti akutumiza ana awo
ku sukulu ngati njira
imodzi yothetsera vuto la
maukwati a ana. n
Boma limanga sukulu
zaluso zitatu ku Machinga
C
H
I
T
H
U
N
Z
I
:

N
A
T
I
O
N

L
I
B
R
A
R
Y
Ntchito za manja zimathandiza
kuthetsa umphawi
3 16 SEPTEMBER 2014
6 ZA ANA NDI CHINYAMATA
CYO izindikiritsa
anthu za kusintha
kwa nyengo
Youth work camp ingachepetse
mavuto osowa ntchitoNYCOM
B
ungwe loyanganira
achinyamata la
National Youth
Council of Malawi
(Nycom) lapempha boma
kuti liyese kugwiritsa
ntchito njira yomwe
akuyitcha youth work
camp pothetsa mavuto
omwe achinyamata
akukumana nawo kaamba
ka kusowa kwa ntchito
mdziko muno.
Cholinga cha youth
work camp chimakhala
k u s o n k h a n i t s a
achinyamata odzipereka
kuti akagwire ntchito
zotukula madera awo
mo s a y e mb e k e z e r a
chilichonse kupatula
maluso osiyanasiyana
omwe amaphunzira
pogwira ntchito.
Ku Malawi kuno, bungwe
loyamba kugwiritsa ntchito
njira imeneyi linali la
Active Youth Initiative
for Social Enhancement
(Ayise) mchaka cha 1999
ndipo lidamanga zipinda
WATIPASO MZUNGU JNR
zophunziriramo komanso
malo ochezera achinyamata
madera ochepa chabe.
Ndipo polankhula
Lolemba lathali atayendera
ntchito yomanga
Thyolo Multipurpose
Learning Centre,
yomwe idamangidwa
ndi achinyamata
ongodzipereka miyezi inayi
yapitayo, mkulu wa Nycom,
Ntchito za manja zitha kuthetsa ulova
mdziko muno
WATIPASO MZUNGU JNR
Bungwe la Concerned Youth Organisation
(CYO) masiku apitawa lidachita misonkhano
kumsika wa Limbe ndi malo ozungulira pofuna
kuzindikiritsa anthu za kufunikira kosamala
zachilengedwe ngati njira imodzi yolimbana ndi
kusintha kwa nyengo.
Bungweli lidapemphanso anthu kuti atengepo
gawo pa ntchito zobwezeretsa chilengedwe monga
kubzala mitengo komanso kuteteza nkhalango
zomwe dziko lino lili nazo.
Ndipo poyankhula panja pa Pound Shop ku
Limbe, mkulu wa CYO, a Harvey Chimaliro,
adatsindika za kufunikira koti boma ndi
makampani agwirane manja poteteza
zachilengedwe popewa kugwiritsa majumbo ndi
mababu osavomerezeka.
A Chimaliro adati njira imodzi yochepetsera
mavuto omwe Malawi akukumana nawo chifukwa
cha kusintha kwa nyengo ndiye kulimbikitsa
magetsi adzuwa.
Iwo adapemphanso achinyamata kuti atengepo
gawo lalikulu pa ntchito imeneyi.
Ndipo pocheza ndi FUKO pa lamya, mkulu
woyanganira nkhalango mboma la Blantyre, a
Chisomo Comrade Masanjala, adati dziko lino
silingapambane nkhondo yolimbana ndi kusintha
kwa nyengo ngati achinyamata sakutengapo gawo
lalikulu. n
a Aubrey Chibwana,
adati dziko la Malawi
likadatukuka kwambiri
pachuma komanso
chitukuko chikhala kuti
boma lidakhazikitsa
ndondomekoyi maboma
onse adziko lino.
A Chibwana adati
ndondomekoyi ndi yabwino
kaamba koti imalimbikitsa
achinyamata kukhala
ndi mtima wodzipereka
potukula madera awo
mo s a y e mb e k e z e r a
kulipidwa.
Ndi kudzera mu njira
imeneyi, achinyamata
amaphunzira maluso
osiyanasiyana omwe
angathenso kuwathandiza
kudziyimira pawokha
ngati mwayi wantchito
palibe, iwo adatero.
Mkulu wa bungwe
la Thyolo Active Youth
Organisation (Tayo),
a Willard Mwambo,
ati achinyamata 80
ndi omwe adatengapo
gawo pomanga bwalo
la masewero komanso
malo ochezera paboma la
Thyolo. n
Jese ali patchuthi ndipo
ali kumudzi kwawo
kuthandiza makolo ake
ntchito za kumunda.
Iwo akukolola chimanga.
Chaka chino kuli dzinthu,
koma kupusa titha kulonga
njala akuba atamaliza
kukolola mundawu, mayi a
Jese abwekera.
JESE
WOJAMBULA: RALPH MAWERA
APULUMUTSA ANZAKE KU UHULE
Mayiwo aponya maso
kumsewu ndipo awona
mnzake wa Jese yemwe
akuyitana Jeseyo.
Mtsikanayo wavala
thalauzi komanso
kamalaya kothina. Jese
lero ndi tsiku la msika
koma inu tulo mukukolola
chimanga, ndalama mupeza
bwanji?
Mayi Jese akwiya
naye mtsikanayu. Jese
afotokoza kuti mtsikanayo
anayamba ntchito
yogonana ndi amuna kuti
azipeza ndalama. Ife
tayetsa kumuuza kuti
kunja kuno kuli matenda
koma iye ati saopa, amaopa
mimba yokha.

Mayiwo akufuna
kuchitapo kanthu. Jese
ndi mayiwo apita kwa
amfumu kukawauza
kuti atsikana ambiri
akulowa ntchito ya
uhule nthawi ino ya
holide. Muchitepo
kanthu. Mfumu ikwiya
ndi nkhaniyi.
Onse ndi amfumu
ayitanitsa mudzi wonse
kuti alankhule makolo
ndi ana zakhalidwe
limeneli. Mmudzi muno
mwayamba khalidwe
lonyansa, atsikana
mukumapita kumsika
kukachita uhule,
ndithetsa msika ngati
simusintha.
Dzidzidzi Jese ayima
ndipo aloza mmodzi
mwa amayi mmudzimo
amene amauza atsikana
kuti sukulu ilibe phindu
bola azichita uhule.
Pomva mauwa mayiyo
avwandamuka naliyatsa
liwiro kuthawa.
C
H
I
T
H
U
N
Z
I
:

N
A
T
I
O
N

L
I
B
R
A
R
Y
3 16 SEPTEMBER 2014 7
ZAUMOYO
Ebola, kufala ndi
zizindikiro zake
Kodi Ebola ndi chiyani?
Ebola ndi matenda owopsa womwe avuta kwambiri
maiko akumadzulo kwa Africa. Mmbuyomu Ebola
imadziwika ndi dzina loti Ebola Haemorrogic Fever.
Mwa odwala 100 omwe amagwidwa ndi matendawa
90 amamwalira.
Ebola imagwira anthu komanso nyama za ku
ntchire monga anyani.
Matendawa amapezeka koyamba mchaka cha
1976 ku Democratic Republic of Congo komanso
ku Sudan ndipo akatswiri amakhulupirira kuti
kachilombo kofalitsa matendawa kanachokera ku
mileme.
Nanga Ebola imafala bwanji?
Ebola imafala kudzera mmadzitukuta, magazi,
umuna kapena ukaziwotuluka mthupi la
wodwala.
Ebola ithanso kufala kupyolera mu zovola,
zofunda ndi majakisoni akuchipatala ngati zinthuzo
zakhudzana ndi madzi a mthupi la wodwalayo.
Mmene timalemba nkhaniyi nkuti ogwira ntchito
kuchipatala oposa 100 atakhudzidwa kale ndi
matendawa chifukwa chokhudzana ndi odwala.
Izi zachitika kaamba koti ena mwa iwo sanavale
zidazodzitetezera. Bungwe loona za umoyo
pa dziko lonse la World Health Organisation
(WHO) lilipakalikiliki kufotokozera anthu mmene
angapewere matendawa.
Kodi anthu ndi mabanja
ndiwovomerezeka kusamalira odwala?
Bungwe la WHO likulangiza anthu ndi mabanja
kuti asasamalire okha odwala Ebola pa khomo koma
azipita nawo ku chipatala kukalandira chithandizo.
Malingana ndi malipoti a WHO, Ebola ikufalanso
kwambiri pa maliro makamaka anthu akamasambisa
mitembo komanso kukhudzana ndi madzi ochokera
mthupi mwa odwala.
Bungweli likulangiza kuti wodwala ayenera
kusamalidwa ndi achipatala. Achipatalawo ayenera
kuvala zovala zodzitetezera pothandiza wodwalayo.
Akamwalira, ayenera kuyikidwa msanga poopa kuti
mtembo wake upatsira anthu ena matenda.
Kodi zizindikiro za Ebola nzotani?
Wodwala amamva ngati malungo, kufooka,
kupweteka mutu, minofu ndi zilonda pa khosi. Izi
zikapitiria, wodwala amasanza, kutsegula mmimba,
amatuluka zilonda pa khungu, ipyo ndi chiwindi
chake sizigwira bwino ntchito yake. Nthawi zina
odwala amatuluka komanso kusanza magazi n
Akonzekera kulimbana ndi Ebola
P
amene Ebola
ikupitirira kutsautsa
ndi kupha anthu
mmayiko akumadzulo
kwa Africa, bungwe
la Red Cross lati
ndilokonzeka kulimbana
ndi matendawa.
Kukonzekera kwapita
patsogolo kutamveka
mpheketsera zoti Ebola
yafika kale mdziko la
Tanzania lomwe lachita
malire ndi dziko lino.
Mkulu wa bungwe
lothandiza pa ngozi la
Red Cross, a Hastings
Kandaya, ati bungwe lawo
layamba kale kuyendera
ndi kuyanganira zipata
zosiyanasiyana zolowera
mdziko muno.
Tikhuphunzi tsanso
anthu osiyanasiyana
mmaboma onse a
dziko lino zizindikiro
za Ebola komanso
mmene angapewere
matendawa, iwo
anatero.
A Kandaya analankhula
izi pa msokhano
wounikanso malamulo
okhudza ngozi zogwa
mwadzidzidzi omwe
anakhazikitsidwa mchaka
cha 1991 (Disaster
Preparedness and Relief
Act of 1991).
Iwo achenjeza anthu
RACHEL KACHALI
Z
I
T
H
U
N
Z
I
:

N
A
T
I
O
N

L
I
B
R
A
R
Y
Ethel Kamwendo-Banda
Tidzapitiriza sabaya ya mawa
Anamwinowa achokera ku WHO
B
ungwe la Support
for Service Delivery
Integration (SSDI)
posachedwapa linakonza
msonkhano wa nyimbo
wa Moyo ndi Mpamba pa
bwalo la Kamuzu Institute
mu mzinda wa Lilongwe.
Skeffa Chimoto,
Moses Makawa komanso
Simeon ndi Kendall,
omwe amadziwika ndi
dzina loti Anyamata a
zakudya anachita nawo
msonkhanowo.
Aka sikoyamba
SSDI mogwirizana ndi
Mercantile International
ndi Musicians Union of
Malawi (MUM) kuchititsa
msonkhano ngati
Chinamtindi chifika ku mpikisano wa
nyimbo wa Moyo ndi Mpamba
RACHEL KACHALI
onse okhala mmalire
a dziko lino kuti
asamangolora alendo
kulowa mdziko lino
mwachisawawa.
Mukawona mlendo
mufunseni komwe
akuchokera. Nanga ali
ndi zizindikiro za Ebola?
Ngati mukumukayikira
kaneneni ku maofesi
azachitetezo, kuchipatala
kapena ku Red Cross,
anateto a Kandaya. n
womwewu ndi thandizo
lochokera ku bungwe la
USaid.
P o s a c h e d w a p a
bungweli linachititsanso
msonkhano ngati
womwewu mogwirizana
ndi Lulu, Tiwonge Hango
ndi oyimba ena mu
mzinda wa Mzuzu.
Mu mpikisanowu
oyimba a mzigawo zonse
akupikisana kupeka nyimbo
zofalitsa uthenga wa kulera,
uchembere wabwino,
umoyo wathanzi, ukhondo
ndi uthenga wokhudza
malungo, kunyentchera,
kutsekula mmimba ndi
matenda ena.
Mmodzi mwa
akuluakulu a SSDI, a Joel
Suzi, anati mpikisanowu
ndi njira imodzi yosinthira
umoyo wa anthu mdziko
muno.
Tikudziwa kuti
nyimbo zimasintha anthu.
Cholinga chathu ndi
kutukula miyoyo ya anthu
mdziko muno kudzera mu
nyimbo, anatero a Suzi.
Iwo anati oyimba
omwe achite bwino mu
mpikisanowo, chimbale
chawo chidzajambulidwa
mwaulere komanso
adzakhala ndi mwayi
woyimba ndi akazembe
a kampeni ya Moyo
ndi Mpamba monga
Skefa Chimoto, Ethel
Kamwendo-Banda ndi
Lulu.
Mpikisano ngati
womwewu uchitikanso
mchigawo cha kummwera.
Tidzatsendera zonse
pakatha sabata imodzi
mchigawo chapakati
pamene tidzayitane oyimba
onse omwe achita bwino,
anatero a Suzi.
A Limbani Silungwe a ku
Mercantile International
womwe akukonza nawo
mpikisanowu anati ndi
wokondwa ndi momwe
anthu akuwulandirira
mpikisanowu.
Kupatula mpikisanowu,
SSDI yakhazikitsanso
sewero lotukula miyoyo
ya anthu lomwe
likuulutsidwa pa mawailesi
a mdziko muno. Bungweli
likuperekanso mabuku a
za umoyo a mChichewa,
Chitumbuka ndi Chiyao. n
Skefa Chimoto
3 16 SEPTEMBER 2014
8
ZAULIMI NDI CHILENGEDWE
ndi ANDREW SAUKANI
ZACHILENGEDWE
Doko lililonse la nsomba mdziko muno liri pansi
pa ulamuliro wa mfumu.
Pakakhala milandu pakati pa asodzi, mfumu ya
mderalo mothandizana ndi komiti yoyanganira
usodzi mderalo ndi amene amaweruza.
Chilichonse chochitika padoko, mfumu ya
mderalo imadziwitsidwa. Pamene zambiri
zakambidwa zokhudza usodzi wa nsomba
pogwiritsa ntchito zikhulupiriro za makolo
pa chisumbu cha Mbenji ku Salima, zonsezo
nzosatheka popanda utsogoleri wabwino.
Chisumbu cha Mbenji chili pansi pa utsogoleri
wa Mfumu Msosa. Mfumuyi imatsogolera
mafumu angonoangono (anyakwawa) a mdera
lake pothira nsembe yothokoza komanso
kupempha mizimu kuti ipereke nsomba zambiri
komanso kuti usodzi uchitike mwamtendere
opanda ngozi.
Ngati njira imodzi yopititsira patsogolo usodzi,
chisumbu cha Mbenji chimatsekedwa ku ntchito
za usodzi kuyambira mu Disembala mpaka Epulo
pofuna kupatsa nsomba mpata woberekana.
Pakakhala mwambo wotseka kapena kutsegulira
usodzi pa chisumbu cha Mbenji, Mfumu Msosa
ndiyo imatsogolera mwambowo ngakhale
akuluakulu a boma amayitanidwa kudzakhala
nawo.
Mfumu Msosa imakhala ndi mphamvu
yovomera kapena kukana mfundo zosiyanasiyana
zomwe makomiti oyendetsa usodzi amakonza.
Asodzi omwe sakutsata malamulo
amawathamangitsa kapena kuwalamula kulipira
chindapusa.
Popeza nsomba zimafa zambiri komanso
zowoneka bwino, asodzi amayesetsa kusunga
bata ndi mtendere pakati pawo kuti asasemphane
ndi zabwino zochokera ku Mbenji chifukwa
kukhalitsa mderalo kumatengera kutsata
mwambi uja amati chakwanu leka.
Zakatangale ku Mbenji kulibe chifukwa Mfumu
Msosa mothandizana ndi makomiti oyendetsa
usodzi amawonetsetsa kuti mchitidwewu
sukuchitika. Opezeka akulandira ziphuphu,
amachotsedwa udindo ndipo akakhala msodzi,
amaunikiridwa muuni kuti azipita kwawo. n
Mfumu Msosa
ikugwira ntchito
yotamandika
Boma lati kusintha kwa
nyengo kukusokoneza
ntchito za umoyo,
chitukuko ndi chuma
mdziko muno.
Nduna ya
zachilengedwe, a Atupele
Muluzi, auza FUKO
posachedwapa kuti
ana, amayi, okalamba,
olumala ndi odwala ndiwo
amavutika kwambri ndi
kusintha kwa za nyengo
ndi zotsatira zake monga
chilala ndi kutsefukira
kwa madzi.
Kusintha kwa nyengo
kukusokoneza chitukuko
Iwo anati Malawi
ikuzunzikabe ndi mavuto
aza chilengedwe ngakhale
yakhala ikukhazikitsa
n d o n d o m e k o
z o s i y a n a s i y a n a
zochepetsera mavuto
omwe amadza ndi
kusintha kwa nyengo.
A Muluzi ayamikira
polojeketi ya za nyengo
ya Ecosystem Based
Adaptation for Food
Security (Ebafos) yomwe
iyambe posachedwa
mmayiko a Malawi,
Zambia ndi Mozambique.
Ebafos ikulandira
thandizo kuchokera ku
bungwe la za nyengo
la United Nations
Environment Programme
(UNEP).
Nzosangalatsa kuti
dziko la Malawi ndi
limodzi mwa mayiko
omwe apindule ndi
Ebafos yomwe cholinga
chake ndi kupereka
thandizo logwirira
ntchito zosiyanasiyana
zoteteza chilengedwe
ndi chakudya, anatero a
Muluzi.
Iwo anati Ebafos
ikuchepetsa zina mwa
zovuta zomwe amakumana
nazo pa ntchito yoteteza
chilengedwe.
Richard Munang,
yemwe anayimira UNEP,
anati Ebafos ithandiza
dziko lino kusunga
chakudya ndi kusamalira
chilengedwe.
Kupyolera mu
Ebafos, ntchito
zosamalira madzi,
kuteteza mitengo, ulimi
wa mleranthaka ndi zina
zothandiza kulimbana
ndi kusintha kwa nyengo
zikhala zikuchitika,
iwo anatero. n
C
H
I
T
H
U
N
Z
I

H
O
L
Y
C
E

K
H
O
L
O
W
A
Mwale: Mbatata imadyetsa
RACHEL KACHALI
A
limi a mbatata
mboma la
Zomba akusimba
lokoma chifukwa cha
phindu lochuluka lomwe
akulipeza akagulitsa
mbewu zawo.
Mmodzi wa alimi amene
akupindula ndi mbatatayi,
a Lens Mwale, adafotokoza
ku chionetsero cha
za ulimi chomwe
chidakonzedwa ndi
bungwe la Blantyre Synod
Health and Development
Commission (BSHDC)
kuti mbatata ndi mgodi
wa ndalama.
Bungweli likuphunzitsa
alimi mmene angapititsire
patsogolo ulimi wawo
kuti azipeza phindu
lochuluka.
A Mwale adafotokoza
kuti kusamalira bwino
mbatata ndikumene
kumachititsa kuti mlimi
azimva kukoma ndi
phindu lochokera mu
mbewuyi.
Chinsinsi changa
ndi chakuti ndimabzala
mbatata yanga
nthawi yabwino. Izi
zimandithandiza kuti
mbatata yanga yikule mu
chinyontho chabwino
chimene chimasungunula
michere yofunikira kuti
ikule bwino, adatero a
Mwale.
Mlimiyu adafotokoza
kuti mbatata ili ndi
ubwino wambiri chifukwa
simafuna feteleza kuti
ichite bwino.
Mlangizi wa za ulimi
mbungwe la BSHDC,
a Wellings Mwalabu,
adayamikira anthu a
mbomali poyika mtima
pa ulimi komanso kaamba
kofuna kuphunzira nzeru
zozama za ulimi.
Masiku ano nyengo
Akupha makwacha ndi mbatata
HOLYCE KHOLOWA
ikusintha kotero mbewu
zambiri zikusintha
mukaberekedwe kake
kotero ndi bwino kuti alimi
akhale tcheru kusakasaka
njira zamakono zimene
angamagwiritse ntchito
pa ulimi wawo kuti azipha
makwacha wochuluka,
adatero Mwalabu.. n
VOL. 5 NO. 18 3 16 SEPTEMBER 2014
Kukwaniritsa ufulu wolankhula zakukhosi Kukwaniriska wanangwa wakuyowoya vyakusingo
JOHN CHIRWA
M
longozgi wa charo
chino, ba Peter
Mutharika, bati
bakukhumba kuti
bafufuze uko kulikuya makopala
ghakuzengera msewu wa Jenda-
Edingeni.
Mazgo agha ghiza pati
pajumpha madazi ghachoko waka
bina Mzimba, chomenechomene
abo bakukhala pa Jenda Trading
Centre, bati badinginyikira
FUKO kuti palije icho
chikuchitika pamsewu uwu
nangauli boma laperekapo
ndalama zakugwirira nchito iyi
kunyuma uku.
Ndipo pakuchezga na FUKO
mu nyuzipepala yithu yapa
August 20 chilimika chino, ba
Chatsalira Phiri bakapempha
boma kuti likumbukire kubikamo
makopala ghakunozgera
msewu wa Jenda-Edingeni mu
ndondomeko yakhe ya chuma
ya chilimika chino na chilimika
chikwiza.
Ba Phiri bakati banthu
bakufumira chigaba bamba
kugongowa na umo boma
likwendeskera nchito yakunozga
msewu uwu, chomenechomene
pakughanaghanira nyengo iyo
yajumphapo kwambira apo
Ndalama za Jenda-Edingeni Road zilikuyankhu?
MUTHARIKA WAFUMBA
likamba kupangana za msewu
uwu.
Iwo bakakoleranako na
Inkhosi ya Makosi Mmbelwa
V abo bakafumba ulongozgi
wa Peoples Party (PP) pasi ba
Joyce Banda kuti ulongosole
za uko kulikuya makopala gha
msewu uwu.
Tikumanya kuti makopala
ghakuzengera msewu uwu
ghakaperekeka. Kwene icho
tikumanya chara nchakuti: Kasi
makopala agha ghali kuluta
nkhuni? bakayowoya ntheura
ba Mmbelwa V ndipo nkhani iyi
tikayilemba mu FUKO ya pakati
pa 5 na 18 March chilimika
chino.
Ndipo pakukoleranako na
madandaulo gha bina Mzimba,
ba Mutharika bakaphalira
banthu abo bakaluta ku ungano
wawo wachisanisani uwo
ukachitikira mu msumba wa
Mzuzu madazi ghajumpha agha
kuti nawoso mbakukhwaskika
na umo nchito iyi yikwendera.
Iwo bakati nawoso
mbakuzizwa ndipo bakukhumba
kumanya uko kulikuya ndalama
izo boma likabikanga mmabajeti
ghakhe ghakumasinda uku.
Kwene mlongozgi uyu
wakaphalira banthu aba kuti
makopala ghanyakhe ghalipo
kale ghakugwirira nchito iyi.
Makopala ghamsewu
uwu ghalipo kale. Kwene
nkhukhumba kuti nifufuze
dankha kuti ndalama izo boma
likabika palwande kunyuma uku
zilikwenda uli, bakati ntheura
ba Mutharika.
Iwo bakati kuti chigaba
chakumpoto chitukuke
pakukhumbikwa kuti nchito
za vyakuzengazenga zilute
panthazi.
Iwo bakati ichi ndicho
chifukwa boma labo
likukhumba kuzenga msewu
wa Mzimba-Kafukule, Nkhata
Bay-Mzuzu, Rumphi-Nyika,
Chikangawa-Nkhata Bay na
Jenda-Edingeni.n
Mutharika: Munyakhe wakwenera kulongosola uko kuli
ndalama za msewu uwu
C
H
I
T
H
U
T
H
U
Z
I
:

N
A
T
I
O
N

L
I
B
R
A
R
Y
Nchito yakuzenga
yunivesite ya
Mombera yambenge
chilimika chino
Mlongozgi wa charo chino, ba
Peter Mutharika, bati bakukhumba
kwamba
na kuzenga sukulu ya univesite
ya Mombera mboma la Mzimba
pambere
bandazenge sukulu zinyakhe
zinkhonde.
Ba Mutharika bakayowoya
ivi pa ungano wachisanisani wa
chipani cha
Democratic Progressive Party
(DPP) mu msumba wa Mzuzu.
Iwo bakati mu ndondomeko
ya chuma cha charo chino iyo
bimiliri ba ku
Mphara ya Malango bambenge
kudumbirana sabata yikwiza,
boma lasidako
kale makopala ghakwambira
nchito iyi.
Ba Mutharika bakatiso nchito
yakunozgekera kuzenga sukulu
iyi
yitolenge miyezi 6 panji 12,
kwene nchito yakuzenga yitolenge
vilimika
vitatu.
Pala tamala kubika
ndondomeko zakunozgekera
kuzenga nakusanga malo,
tambenge kuzenga. Nchito
yakuzenga sukulu iyi yitolenge
vilimika
vitatu, bakayowoya ntheura
ba Mutharika.
Iwo bakalomba mafumu kuti
basange malo agho sukulu iyi
yingakazengekako. n
JOHN CHIRWA
3 16 SEPTEMBER 2014
2
MALONJE
VYA MCHARO
NYUZIPEPALA YINUYINU YAWEZI
Nyuzipepala iyi yikumufkani mwawezi. Usange mwabazga
yisungani makora kuti banyinu nabo bizakabazgepo.
Fumbirirani uko yikufkira mchigaba chinu ndipo
mubazgenge nyengo zose. Usange muli na makani
ghakuti tilembe munyuzipepara iyi lemberani kwa:
Mnozgi wa FUKO, Nation Publications Limited
P. O. Box 30408, Chichiri, BLANTYRE 3.
Bright Kumwenda 088 8 209 027 bkumwenda@mwnation.com
Gift Mashiri (Blantyre) 088 1 762 272 gsibale@mwnation.com
Enala Banda (Lilongwe) 088 8 209 546 ebanda@mwnation.com
Rita Banda (Zomba) 099 1 889 844 ritabanda2@gmail.com
John Phiri (Mzuzu) 088 4 248 747 salesmzuzu@mwnation.com
MNOZGI
MALONDA
Kukwaniriska wanangwa wakuyowoya vyakusingo
Kukwaniriska wanangwa wakuyowoya vyakusingo
Mafumu, lekani
ulyezi pa yunivesite
ya Mombera
Moto wabuska msika wa Karonga
P
ati pajumpha mwezi
umoza pela kufuma
apo misika ya Mzuzu
na Tsoka ku Lilongwe
yilikupya na moto, msika
wa Karonga nawo wapya
sabata yamala.
Muyowoyeri wa bapolisi
mboma ili, ba Enoch
Livason, bati moto uwu
wananga mphepete yimoza
ya msika uwu.
Iwo bati moto ukamba
mushopu chimoza
chifukwa cha suzgo la
magesi ndipo ukagozga
mashopu ghanyakhe
ghakufupi nayo.
Mwabi bapolisi na
bakuzimwa moto bakiza
lubiro, lekani mashopu 10
pela ndigho ghalikupya,
bati ntheura ba Livason.
Mlala wa mavenda
pa msika wa Karonga,
ba Godwin Ghambi,
badandaula na moto uwu.
Iwo bati nangauli banthu
bakukhwafyika mbachoko,
nivyachitima kuti banthu
aba bataya katundu wabo.
Nchipusu chara kuti
munthu wasange makopala
ghakwambira bizinesi. Umo
vilili apa nikuti bakwenera
kwambiraso kupenjapenja
makopala ghanyakhe. Ise
tikulira nabo munyengo
iyi, bayowoya ntheura ba
Ghambi.
Aka nkhakwamba chara
kuti moto ubuske misika
mcharo chino miyezi
yajumpha iyi.
Kufuma mu April kufika
sono, moto wabuska msika
wa Mzuzu kabiri na msika
wa Tsoka ku Lilongwe.
Mlala wa mavenda
kuchigaba chakumpoto, ba
Stanley Simbeye, balomba
mavenda kuti ghazenge
nanjerwa nyumba
zakuguliskiramo vinthu
kuti bavikilire katundu
wabo munyengo ya moto.
Iwo bati nchakusuzga
kuti katundu wapone
mumashopu agho
ghazengeka na makuni
panji vigwagwa.
Sabata yamala, ba
Opportunity Bank Malawi
(OBM) bakafyula masozi
mavenda ghaku Mzuzu
na makopala ghakukwana
K2.6 miliyoni.
PaChitumbuka pali mazgo ghakuti: Kususka galu
nkhujimako. Pa ulendo wakhe wakumpoto madazi
ghajumpha agha, pulezidenti wacharo chino, ba
Peter Mutharika, wakapangana kuti boma lawo
ndakunweka kwambapo nchito yakuzenga yunivesite
ya Mombera.
Kwambura kukayikira, iyi ni nkhani yakukondweska
chomene kwa binampoto abo bakudinginyika
nyengo zose boma likubanola chitukuko.
Ntheura, iyi yikwenera kuba nkhani yakunozga
chomene kwa banthu bakumpoto chilimika chino.
Kwene nga ni umo bakayowoyera ba Mutharika,
nchito iyi yingachitika chara pambere mafumu
ghandapereke malo.
Tikumanya kuti chifukwa chakuzirwa kwa sukulu
iyi, fumu yiliyose yibenge na khumbiro lakuti yipereke
malo ghakuti yunivesite iyi yikazengekepo.
Ichi nchiweme. Kwene suzgo lingiza pala tayamba
kuguzana pa uko kukwenera kukazengeka sukulu
iyi.
Ichi ndicho chifukwa tikukhumba titolerepo
mwabi wakulomba mafumu kuti ghaleke ngaba pa
nchito iyi.
Tikuyowoya ivi chifukwa paumaliro mose mwiza
muzamuluza pala mwakutondeka boma latondeka
kuzenga yunivesite iyi chifukwa chakuti mafumu
mwatondeka kukoleranako pa nkhani yamalo.
Ntheura, pempho lithu ndakuti mukoleraneko
kwambura kuguzana pa uko kukwenera kuba
yunivesite iyi. n
Moto ukuwezgera munyuma chitukuko
JOHN CHIRWA
C
H
I
T
H
U
T
H
U
Z
I
:

N
A
T
I
O
N

L
I
B
R
A
R
Y
Mlala wa nchito za banki
iyi, ba Wilson Moleni,
bakaphalira FUKO kuti
mavenda ghakwenera
kuvikilira katundu
wabo ku ngozi zambura
kunozgekera kwizira mu
ndondomeko ya ishulansi.
Iwo bakati mavenda
ghakusanga chanduro mu
ndondomeko iyi chifukwa
munyengo ya ngozi
kampani ya ishulansi
yikubawezgera makopala
agho bataya. n
BUYAZONKE
Iwe, ukuvulula mu
munda namweneko ninda-
vune. Nakukola ndiwe
munkhungu!
3 16 SEPTEMBER 2014 3 VYA MUUSO UWEME
W
upu wakwendeska
visola wa
Malawi Electoral
Commission (MEC) wati
visola vya
makhaunselala mu wodi
ya Mbalachanda mboma
la Mzimba na Zgeba
ku Karonga Nyungwe
vichitikenge mwezi
ukwiza pa October 7.
Visola muvigaba ivi,
kusazgiraposo vigaba
vinyakhe vinkhonde
mchigaba chapakati na
kumwera, vikatondeka pa
May 20 2014.
Ku Mbalachanda,
visola vikatondeka
chifukwa chakuti vikalata
vyakuvotera mchigaba
ichi vikasangika ku Mchesi
mu msumba wa Lilongwe
apo ku Nyungwe na vigaba
vinyakhe, banthu banyakhe
abo bakatolangapo
lwande pa viphalizgano ivi
bakafwa pambele visola
vindachitike.
Kwene pakuyowoya
mchikalata icho MEC
yafumiska, mlala wa wupu
uwu, ba
Maxon Mbendera,
bati visola vichitikenge
pa October 7 muvigaba
vinkhonde na vibiri
mcharo chino.
Ba Mbendera bati MEC
yambenge kupokera
vikalata kufumira kwa abo
bakukhumba kwima pa
visola ivi pa September 9.
Banthu abo bakapereka
kale vikalata ivi muvisola
Visola vyaku Mbalachanda, Nyungwe viliko pa October 7
Mbendera: Tiyeni tinozgekere visola ivi
C
H
I
T
H
U
T
H
U
Z
I
:

N
A
T
I
O
N

L
I
B
R
A
R
Y
JOHN CHIRWA
JOHN CHIRWA
Bapolisi ku Ekwendeni
mboma la Mzimba
balomba mafumu kuti
ghabawovwire pakumazga
msinjiro wa madoda ku
basungwana.
Mlala wa bapolisi
mchigaba ichi, ba Paul
Kachingwe, baphalira
FUKO kuti msinjiro kwa
basungwana mbukulu
mchigaba ichi kwene
suzgo ndakuti banthu
bakuphala chara vya ivi.
Milandu iyi yikumalira
pavindumbirano na
mabanja ghakukhwafyika
pakopa kulengeskana.
Banthu bakuphala kupolisi
chara vya ivi. Kwene pala
mawupu ghamanya vya
ivi, ndipo makani agha
ghakusokoloka.
Ivi vikutipa suzgo
ise chifukwa ikuba kuti
nyengo yajumpha yinandi
kuti tisange ukaboni
wakwenelera kufuma
kuchipatala. Antheura
tikulomba mafumu kuti
ghalabisiske kuti banthu
bakuphala ivi mwalubiro,
bayowoya ba Kachingwe.
Kwene ba Kamukhoti
Mkandawire, fumu
ya mchigaba ichi, bati
banthu banandi bakuchita
ivi chifukwa cha midauko
yamboma ili.
Iwo bati babika malango
ghamvikaya pakumazga
masuzgo agha.
Kwene ba Mkandawire
basinginika na nkharo
ziheni za baukirano
mchigaba ichi, ivyo bati
vikulutiska panthazi
vya pa May 20 balembe
kalata kutimanyiska kuti
bimenge nawo, iwo bati
ntheura.
Iwo bati banalume
abo bakukhumba kwima
nawo pachiphalizgano cha
ukhaunselala bakwenera
kupereka K20 000 ndipo
banakazi baperekenge
K15 000 muvisola vya
makhaunselala.
Muvisola vya bimiliri
ku Mphara ya Malango,
banalume baperekenge
K200 000 ndipo bamama
msinjiro.
Iwo bati baukirano
banandi bakupokera
wovwiri wakwenelera
chara kufuma ku bapapi
babo lekani bakwamba
nkharo zambura
kwenelera. n
baperekenge K150 000.
MEC yaphalazgaso kuti
kufuma pa September
4 mpaka 8, wupu uwu
ulembenge mazina gha
bina Malawi abo balikufika
pavyaka vyakuvotera vya
18 panji kujumpha apo.
Kwene wupu uwu wati
abo bakalembeska kale
bakwenera kulembeskaso
chara kwene barute
kukawona pala mazina
ghawo ghalimo mbuku.
Malango gha charo
chino ghakuphala kuti
MEC yichemeske chisola
chinyakhe pambele
madazi 60 ghadajumphe
kufuma apo visola
vyakwamba
vyatondeka.
Kwene MEC yatondeka
kufiska malango agha
chifukwa visola ivi
vichitikenge pati
pajumpha madazi 140
kufuma pa May 20 na 23
apo
visola mvigaba ivi
vikatondeka.
Visola ivi vichitikengeso
ku chigaba cha Goliati
mboma la Thyolo uko
basolenge mwimiliri wa ku
Mphara ya Malango. Uku
uyo wakaluska, ba Peter
Mutharika, bakasolekaso
kuba mlongozgi wa charo
chino.
Vigaba vinyakhe ni
kumpoto kwa Blantyre,
Lisanjala mboma la
Machinga,
Kandeu ku Ntcheu na
Lifupa ku Kasungu. n
Mafumu ghovwire pakumazga
msinjiro ku basungwana
3 16 SEPTEMBER 2014
4
VYA BAMAMA NA JENDA
MTOLANKHANI WITHU
WATIPASO MZUNGU JNR
Bamama abo bali na masambiro
ghakukwana babalomba
kuti bazakaphalizgane nawo
pavisola vyachiwerezga ivyo
vichitikenge mwezi ukwiza.
Wupu wa Community
Initiative for People
Empowerment (Cipe) wati
charo chino chingakwera
W
upu wa Technical,
Entrepreneurial and
Vocational Education
and Training Authority (Teveta)
wati ukukhumba bomama
banandi basambire maluso gha
nchito za mawoko pakukwezga
nchito zachuma mcharo chino.
Ndipo pakukhumba kufiska
ivi, Teveta yabika ndondomeko
yakusambizga basungwana 60
pa 100 yiliyose mu pulojekiti
yakhe yakusambizga baukirano
bakusuzgika.
Pulojekiti iyi yikuchemeka
kuti Vocational Skill Training
Project for Vulnerable Young
People (VSTP VYP).
Mlala wa Teveta kuchigaba
chakumpoto, ba Conceptor
Nyamadzawo Bamusi, bati
kunyuma uko banalume
banandi ndiwo banguvwirika
na mapulojekiti ghawo
kuluska bomama.
Iwo bati suzgo la kuchepa
kwa banakazi kuti lili mu
mmapulojekiti ghawo
pera chara chifukwa nanga
mungaba mawupu na boma
maudindo ghali mmawoko
gha banalume.
Ndondomeko ya banakazi
60, banalume 40 yikukhumba
kovwira bomama banandi kuti
C
H
I
T
H
U
T
H
U
Z
I
:

N
A
T
I
O
N

L
I
B
R
A
R
Y
Mama kugwira nchito izo kale bakatenge ni za banalume
Cipe yalomba bamama baphalizgane nabo pavisola vyachiwerezga
Teveta yikukhumba bamama
basambire nchito za mawoko
basambire maluso gha nchito
za mawoko. Ndondomeko
iyi yovwirenge kukwezga
bomama mmaudindo
ghakupambanapambana, iwo
bayowoya.
Pulojekiti ya VSTP VYP
yikugwirika mmaboma ghose
mcharo chino na wovwiri
wakufumira ku wupu wa National
Aids Commission (NAC).
Pali chigomezgo chakuti
baukirano 3 600 basambirenge
maluso gha nchito za mawoko
pakati pa vyaka vya 2012 na
2015. n
chomene pa chitukuko pala
bamama banandi bangatola
maudindo.
Wapachitengo mupya wa
Cipe, ba Trintas Manda,
ndiwo bangupereka pempho
ili sabata yamala pa ungano
wachisanisani uwo wupu uwu
wanguchitiska pa sukulu ya
Mabiri.
Ba Manda bakapemphaso
mafumu na banthu babo
kuti bovwire bomama abo
mbakunweka kwizakaphalizgana
pa visola ivi.
Nyengo yakuti ndyale ni
za badada yilikumala. Cipe
yikukhumba kumulombani
mwa bomama mose imwe muli
na masambiro ghakukwana kuti
mwime nawo pa visola ivi.
Tipempheso mafumu kuti
muyezgeske kovwira bomama
abo mbakunweka pakutolapo
lwande pa viphalizgano ivi,
iwo bakadininizga.
Pakuyowoyapo, ba Vileji
Hedemani Mtambalika bakati
ibo mbakunozgeka kusambizga
banthu babo vya uweme
wakubika bomama mu mipando
yikuluyikulu.
Ine nga fumu, nili panyuma
pinu ba Cipe pakukwezga
bomama mchigaba chino,
bakayowoya ba Mtambalika.
Cipe yikugwira nchito zakhe
kwambura wovwiri wa makopala
na chakulata chakulwera
nkhondo banthu pa vitukuko
vyakupambanapambana kwizila
mu ulongozgi wakunowera
waliyose ndipo yili pasi pa
Fumu Mzukuzuku Jere. n
3 16 SEPTEMBER 2014 5 VYA MASAMBIRO
Mwabi wa masambiro ghapachanya wasuzga
JOHN CHIRWA
Kuti munthu wasange
mwabi wamasambiro
ghapachanya madazi
ghano nkhwakusuzga
chomene mwakuti
banthu abo bakukhumba
kusambira vya usambizi
ku Karonga Teachers
Training College
(TCC) nabo mbanandi
chilimika ichi.
Sabata yamala, banthu
bakujumpha 1 200
kuchigaba chakumpoto
kwaboma la Mzimba
bakiza ku sukulu ya
Katoto mu msumba wa
Mzuzu kuti balembe
vilingwa vyakunjirira ku
sukulu iyi.
Yumoza mwa basambizi
abo bakalembeskanga
vilingwa ivi, kwene
wakakana kuti
timuzunule zina, wakati
aka nkhakwamba kuti
banthu bize banandi
nthena.
Iwo bakati mmaboma
ghanyakhe banthu abo
bakukhumba usambizi
bakujumpha 300 chara.
Ise nase tazizikika na
unandi wa banthu abo
bakukhumba usambizi
chilimika chino,
bakayowoya ntheura.
Kwene banthu abo
FUKO yikachezga
nabo bakati mwabi
wamasambiro wasuzga
chomene mcharo chino
lekani bakukhumba
kuluta kulikose uko
mwabi wamasambiro
ukusangika.
Yumoza mwa banthu
aba ni Emmanuel Banda
uyo walikukwera na
W
achibiri kwa
nduna ya
vyamasambiro, ba
Vincent Ghambi, bati
boma likukhumba
kuzenga nyumba zinandi
zakuti basungwana
bagonengemo mu
sukulu zakwendera za
community day secondary
school (CDSS).
Boma, pasi pa muuso
wa mlongozgi wa kale
Joyce Banda, likakanizga
basambiri banakazi abo
balikusolekera ku ma
CDSS kuti bagonerenge
kusukulu kwenekuko
mwakujovwira bekha.
Kwene bakwendeska
nchito za Kalondolondo
iyo ni ndondomeko
yakulabiska umo nchito
zachitukuko chaboma
zikwendera, ba Jephter
Mwanza, bakasuska boma
pamaghanoghano agha.
Ba Mwanza bakati ni
msinjiro ukulu kuti boma
lilekeske chinozgero ichi
chifukwa chikuvwira
basambiri abo bakufumira
kumabanja ghakavu.
Kwene pakuchezga na
FUKO sabata yamala,
ba Ghambi bakati
boma likukhumba
kovwira basambiri
bakumizi pakuzenga
nyumba zinandi
zakuti basungwana
bagonengemo.
FUKO yikabafumba
ba Ghambi pala boma
la ba Peter Mutharika
lisinthenge dango
lakukanizga basungwana
kuti bagonenge ku sukulu
za CDSS mwakujovwira
bekha.
Boma lamba kuzenga
nyumba zakugonamo
basungwana mwakuti
timazge masuzgo agho
bakukumana nagho pa
masambiro mvigaba
vyakumizi. Chasonosono
apa, tajura nyumba
yabasungwana pa sukulu
yimoza ya CDSS ku
Dwangwa.
Unduna wane
n g w a k u k h w a f y i k a
na masuzgo agho
Boma likukhumba kuzenga vipinda
vinandi vyakugonamo basungwana
JOHN CHIRWA
C
H
I
T
H
U
T
H
U
Z
I
:

N
A
T
I
O
N

L
I
B
R
A
R
Y
Basambiri bachanakazi bakusuzgika kusanga malo ghakugona
MANYANI VYA MISONKHO
Wupu waboma wakutola msonkho wa Malawi
Revenue Authority wambapo kulipiska chibuda
kwa beneko ba magalimoto agho ghakhala madazi
ghakujumpha khumi (10) paboda kwambura
kuwombola.
Malinga ni mlala wa MRA, a Raphael Kamoto,
mwenecho wa galimoto yiliyose iyo yakhala
paboda kwakujumpha madazi 10 wakwenera
kulipa ndalama zakukwana K5 000 pa dazi lirilose
lakusazgirapo.
Banthu banandi bakutemwa kugula galimoto
nakuzileka paboda ivyo vikuchitiska kuti malo
ghakusungira galimoto ghachepe. Ba MRA
bakweneraso kulabisiska kuti galimoto izo zili
pamaboda ghakhe zili na chivikiliro.
Wupu wa MRA ukutaya makopala ghanandi
chomene pa nchito yakusunga chifukwa galimoto
izi bakukhomera waka msonkho wakunjirira
mcharo chino, kwene kusunga chara.
MRA yikumanyiska banthu bose abo bakuchemeska
panji bakukhumba kuchemeska galimoto
kufuma kuvyaro vyakuwalo kuti banozgekerenge
mwakufikapo (pakusunga makopala
ghakuwombolera) pambere bandachemeske
galimoto.
Ivi vikovwira kuti mumanye kuwombola galimoto
zinu mwalubiro nakuti muleke kubadala chibuda.
Pala mukukhumba kumanya vinandi pa nkhani iyi,
lutani ku ofesi yiliyose ya MRA iyo yili mchigaba
chinu kuti bakamupeni ndondomeko yakwenelera
pakuchemeska galimoto kuwalo. Nchakwenerera
kumanya vya msonkho uwo mukwenera kukhoma
pa galimoto iyo mukukhumba kugula. n
Chibuda chifukwa
chakutondeka
kuwombola
galimoto
munyengo yakhe
basungwana bakukumana
nagho chifukwa cha
chinozgero chakuti
bagonenge ku sukulu
mwakujovwira bekha,
bati ntheura ba Ghambi.
Kwene iwo batondeka
kuzgorapo pala boma
lidabude pakukanizga
basungwa kugonera
mu sukulu za CDSS
mwakujovwira bekha. n
mapointi 13 pa vilingwa
vya MSCE.
Iye wati wakukhumba
kusangirathu malo
ghamasambiro ku TTC
chifukwa wakumanya
chara pala wangazasanga
mwabi wakuluta kukoleji
za University of Malawi.
Tabanthu ise
tikukhumba kuluta ku
koleji tilipo banandi
lekani nkhukhumba
kusangirathu mwabi wa
sukulu kulekana nakuti
nikhalenge waka, wati
ntheura Emmanuel. n
3 16 SEPTEMBER 2014
6 BANA NA BAUKIRANO
Banalume bakukhumba
kuba balezi chara
W
upu wakugwira
nchito zakuchiska
banthu
zakukhumbikwa kwa
sukulu zamkaka wa
Association of Early
Childhood Development
in Malawi (AECDM)
wadandaula nakuchepa
kwa balezi bachanalume
mu sukulu izi.
AECDM yikugwira
nchito izi mmaboma gha
Rumphi, Nkhata Bay,
Mchinji, Ntcheu, Mwanza
na Neno na wovwiri
wakufumira ku thumba la
Tilitonse.
Sabata yamala, AECDM
yikapereka masatifiketi
ku bamama 19 abo
bamalizga masambiro gha
nchito izi kwa masabata
ghabiri ku Karonga na
Mzuzu.
Wakwendeska
nchito za wupu uwu,
ba Ruth Makwakwa,
bakaphalira FUKO kuti
muvigaba vinandi kulije
balezi banalume ivyo
JOHN CHIRWA
bati vikunjizga pasi
masambiro agha.
Banthu banandi
bakuwona nga kuti
nchito ya ulezi nja
bamama pera. Nchito iyi
nja munthu waliyose,
bakayowoya ntheura ba
Makwakwa.
Nchito yakukwezga
masambiro ghabana
kuti yikukhumba
kubasambizga pera chara.
Pali vinthu vinyakhe
ivyo vikukhumba
wovwiri wa banalume
nga kuzenga vipinda
vyakusambizgiramo
na kunozga vilwero
vyakusambizgira bana.,
iwo bakasazgirapo. n
C
H
I
T
H
U
T
H
U
Z
I
:

N
A
T
I
O
N

L
I
B
R
A
R
Y
Nchito yakusambizga bana nga aba njatose
Jese wali paholide ndipo
walikukaya kwake kovwira
bapapi bakhe nchito
zakumunda. Chilimika
chino kuli vuna, kwene pala
tapusa vuna iyi yingamalira
kwa bankhungu chifukwa
chakuchedwa kuvuna
lubiro, anyina Jese
bayowoya ntheura.
JESE
WOJAMBULA: RALPH MAWERA
WAPONOSKA BANYAKHE KU UHULE
Anyina bakhe balabiska
kumsewu ndipo bawona
munyakhe wa Jese
wakumuchema Jese.
Msungwana wavwala
buluku kweneso kalaya
kakufyenya. Jese,
mhanyauno ndi dazi
lamsika kwene imwe
mbwenu mukutangwanika
na kuvuna ngoma, ndalama
musangenge uli?
Anyina Jese bakwiya
naye msungwana yura.
Jese walongosola
kuti msungwana yura
walikwamba nchito ya
uhule kuti wasangenge
makopala. Ise tayezga
kumuphalira kuti kuno
kucharo kulikuwa matenda,
kwene iye wakuti wakopa
chara. Bati iye wakopa
nthumbo yekha.
Jese na anyina baluta
kwafumu kukabaphalira
kuti basungwana
banandi bakwamba
uhule nyengo yaholide.
Muchitepo kanthu.
Afumu bakwiya na
nkhani iyi.
Wose na afumu
bachemeska muzi
wose kuti bayowoye
na bapapi na bana vya
nkharo iyi. Mmuzi uno
mwawa nkharo yiheni,
basungwana mukuluta
kumsika na chakulata
chakukachita uhule.
Nimazgenge msika pala
mukuleka kusintha.
Jese wayimilira ndipo
walongora yumoza mwa
bamama ba mmuzi uwu
kuti ndiwo bakuphalira
basungwana kuti
bachitenge uhule ndipo
mama uyu wachimbira
wati wapulika mazgo
agha
Mlala wa Malawi Prison Service (PS) mchigaba
chakumpoto, ba Mahlatini Moyo, bati baukirano
abo bakugwira ukayidi bakwenera kusambira
maluso ghakupambanapambana kuti baleke kuba na
maghanoghano ghakuchimbira.
Ba Moyo bayowoya ivi kulondezga nchito iyo wupu
wa Music Crossroads Malawi ukugwira ku gadi ya
Mzuzu.
Music Crossroads yikusambizga baukirano abo
bali mugadi maluso ghakupambanapambana nga
nkhwimba na kuvina kwizila munchito yakhe iyo
yikuchemeka kuti Young in Prison (YIP).
Munchito iyi, wupu uwu wasambizga baukirano
1 000 mu gadi za Mzuzu, Kachere ku Lilongwe na
Bzyanzi ku Dedza.
Ba Moyo bati nchito iyi njakukhumbikwa chifukwa
yikovwira baukirano kusanga chakuchita mnyengo iyo
bali mgadi.
Baukirano banandi bakusoba chakuchita mugadi
mwakuti banji bakughanaghana vyakuchimbira.
Tikukhumbisiska kuti baukirano aba basange
chakuchita kuti baleke kughanaghana vyakuchimbira,
bayowoya ba Moyo.
Iwo batiso masambiro agha ghangovwira bakayidi
kukasanga nchito kuwalo pala bamalizga ukayidi
wawo.
Yumoza mwa baukirano abo bapokera masambiro
agha, Michael Phiri, wati wakukhumba kufumiska
sumu mwakuti wasangirengemo makopala.
Music Crossroads yikamba nchito ya YIP mchilimika
cha 2009 wupu uwu wati wawona masuzgo agho
baukirano bakukumana nagho mugadi. n
Baukirano basambire
vyamaluso mu gadi
JOHN CHIRWA
3 16 SEPTEMBER 2014 7
VYA UMOYO
Ebola, kuthandazgika
na vimanyikwiro vyakhe
W
umba wabanthu
abo bakukotoleska
m m a b o m a
ghakumpoto nguchoko
chomene kulingana na
umo unduna wa vyaumoyo
ukaghanaghani ranga,
wupu wa Jhpiego
wayowoya.
Jhpiego yikuchitiska
nchito ya ukotoli wa
banalume wakuchipatala
mmaboma gha Karonga,
Mzimba, Kasungu,
Lilongwe, Salima,
Mangochi na Zomba.
Kwene apo nchito iyi
bakuti yikwenda makora
mmaboma ghakumwera,
vinthu vili ntheura chara
kumpoto uko bakuti
banalume bakuwoneka
kuti mbakunweka chara
kuti bakotoleske.
Yumoza mwa
balalabalala ba wupu uwu,
uyo wakalomba kuti tileke
kuzunula zina lakhe,
wakati ivi vili ntheura
chifukwa chavigomezgo.
Tikugomezga kuti
baNgoni panji baTumbuka
bakogomezga mukukotola
chara kulekana na
banyithu bamchigaba
chakumwera, iwo
WATIPASO MZUNGU JNR
balongosola.
Chilimika chamala,
apo madokotala
ghakachiskanga badada
kuti bakatheneske
(vasectomy) nga nthowa
yimoza yakuchepeskera
Kasi Ebola nchichi?
Ebola ni matenda ghakofya agho ghakusuzga
chomene vyaro vyakuzambwe (kumise) kwa Africa.
Kunyuma uku, Ebola yikamanyikanga kuti Ebola
Haemorrogic Fever. Mwa balwari 100 abo bakhwaskika
na matenda agha, 90 bakufwa.
Ebola yikukola banthu kweneso vinyama
vyakuthengere nga minkhwere.
Matenda agha ghakasangika kakwamba mchilimika
cha 1976 ku Democratic Republic of Congo kweneso
Sudan ndipo nkhwantha pa vyaumoyo bakugomezga
kuti kachibungu ako kakuthandazga matenda agha
kakafumira ku kasuska.
Kasi Ebola yikuthandazgika uli?
Ebola yikuthandazgika kwizila mu thukuta, ndopa
panji wanakazi wakufumira kwa mulwari.
Ebola yingamanya kuthandazgikaso kwizila mu
vakuvwala, vyakudika kweneso jekeseni wakuchipatala
pala vinthu ivyo vyakhwaskana na maji ghamthupi la
mulwari.
Apo tikalembanga nkhani iyi, bakugwira nchito
kuchipatala bakujumpha 100 bakaba kuti bakhwaskika
kale namatenda agha chifukwa chakukhwaskana na
balwari.
Ivi vyachitika chifukwa chakuti banyakhe mwa
ibo bakavwalanga mwakujivikilira chara. Wupu wa
vyaumoyo pacharo chose wa World Health Organisation
(WHO) uli mkati kuchiska banthu umo bangalewere
matenda agha.
Kasi banthu na mabanja
ngakuzomerezgeka kupwelerera balwari?
Wupu wa WHO ukuchiska banthu na mabanja kuti
bangatolangapo lwande chara pakupereka wovwiri kwa
balwari kweneso kuti bachimbirirenge na abo basangika
na matenda agha kuchipatala.
Malinga ni malipoti gha WHO, Ebola
yikuthandazgikaso chomene panyifwa,
chomenechomene pala banthu bakugeziska chitanda
(thupi la wakufwa).
Wupu uwu ukuchiska banthu kuti balwari bakwenera
kupwelerereka na bachipatala pera. Bachipatala
bakwenera kuvwala vyakuvwala ivyo vingovwira
kujivikilira ku matenda agha.
Kasi vimanyikwiro vya Ebola nivichi?
Mulwari wakupulika phungo (malaria), kusoba
nkhongono mthupi, kubinya kwamutu na minofu,
kweneso vilonda vyapasingo.
Ivi pala vikupitirira, mulwari wakuukura (kubokola),
kujura munthumbo, kufuma vilonda pathupi, ziso na
chibindi chakhe vikuleka kugwira nchito yakhe.
Nyengo zinyakhe, mulwari wakufuma panji kubokola
ndopa.
Tilutirizgenge sabata yamachero
Chipatala cha Ekwendeni
mboma la Mzimba
chati chikukhumba
kusazgirapo unandi wa
banthu abo bakupokera
wovwiri mu nchito zawo
zakumazga ukavu wa
banthu abo bakhwafyika
na matenda gha Edzi.
Munchito iyi, chipatala
cha Ekwendeni icho chili
pasi pa mpingo wa CCAP,
chikufikira banthu 75 000
na makopala ghakukwana
K39 miliyoni pachilimika
chilichose.
Kwene mlala wa nchito
iyi, ba Esther Lupafya,
baphalira FUKO kuti
makopala agha nganandi
chomene mwakuti
Bakukhumba kumazga ukavu
uwo ukwiza chifukwa cha edzi
unandi wa bana abo banja
limoza likwenera kuba
nawo, badada banandi
mboma la Mzimba na
maboma ghanyakhe
ghakumpoto ghakakana
nthowa iyi.
Ibo bakuti bakakana
nthowa iyi chifukwa
chachigomezgo chakuti
munthu wakwenera kuba
na bana banandi kulongola
kuti ni mwanalume
wanadi. n
C
H
I
T
H
U
T
H
U
Z
I
:

N
A
T
I
O
N

L
I
B
R
A
R
Y
Chimoza mwa vipatala ivyo vikupereka nthowa zakulera ku mabanja
Nchito yakukotoleska
yasuzga ku Mzimba
b a k u g h a n a g h a n a
vyakufikira banthu
banyakhe abo bangapenja
wovwiri uwu.
Nchito iyi yikamba
mchilimika cha 1990
kwene muchilimika cha
2005 ndipo bakasanga
wovwiri wa makopala
kufuma ku Department of
Foreign Affairs, Trade and
Development (DFATD)
na Presbyterian World
Service and Development
(PWS&D).
Kufika sono, nchito
iyi yapereka wovwiri
JOHN CHIRWA
wa masambiro ku bana
bakukwana 1 000.
Kweneso, bazengera
nyumba banthu bakavu.
Chilimika chamala pela
bazenga nyumba zitatu.
Bapereka wovwira wa
chakulya ku mabanja na
mawupu agho ghakulera
bana balanda bakukwana
912.
Bazengaso nyumba
zakukwana 181
zakuti bana balanda
bakhalengemo. Nchito
iyi yikovwiraso bamama
na makopala kuti bambe
mabizinesi mwakuti
bavwire bana balanda.
Ba Lupafya bati chilato
cha nchito iyi nkhovwira
bana balanda kuti bakule
na nkharo zakwenelera.
Tili na malo
agho baukirano
bakusambirako maluso
ghakupambanapambana
pakubapa chakuchita
mwakuti baleke nkharo
ziheni. Kweneso, mu
nyumba za bana balanda,
tikupereka wovwiri uwo
bana aba bakusobelwa,
bayowoya ba Lupafya. n
3 16 SEPTEMBER 2014
8VYA ULIMI NA CHILENGIWA
na ANDREW SAUKANI
VYA CHILENGIWA
Unilia yambenge kusambizga
balimi bamvikaya
U
nivesite ya
Livingstonia (Unilia)
mboma la Rumphi
yati yikukhumba kujura
koleji yakuti yisambizge
nchito za ulimi kwa
banthu bakumizi.
Wachibiri kwa mlala
wa sukulu iyi, ba Yohane
Nyirenda, baphalira FUKO
pachisulu kuti koleji iyi
bayijurenge ku Lusangazi
mu msumba wa Mzuzu.
Tikukhumba kuti
sukulu iyi yisambizge
banthu bakukaya vya
ulimi wa somba, viweto,
makuni na vyakulya.
Kweneso, basambizi bakhe
bazamwenderanga kumizi
kusambizga vya ivi,
bayowoya ba Nyirenda.
Ba Nyirenda bati
bambenge nchito izi
chilimika chikwiza.
Kwasono tikupenjapenja
dankha makopala ghakuti
tizengere nyumba
z a ku s a mb i z g i r a mo ,
kweneso tikukhumba kuti
tikhazikiske visambizgo
vyakhe. Chilimika chikwiza
tambenge na masambiro
JOHN CHIRWA
Pala balovi bayambana, fumu yamchigaba icho
mwakukoleranako na komiti yakuwona vyaulovi
pa BVC ndiwo bakwenera kweruzga mphindando
izi. Chilichose chakuchitika pamalo agho, fumu
yamchigaba icho yikwenera kuchiskika.
Apo vinandi vyayowoyeka vyakukhwaskana
na ulovi wakulera somba pakugwiriska nchito
vigomezgo vyamwaka kwa Mbenji mboma la
Salima, vyose ivi vingachitika chara pala palije
ulongozgi uweme.
Mbenji yili pasi pa ulongozgi wa Fumu Msosa.
Fumu Msosa yili na mlimo wakulongozga
mafumu ghachokoghachoko (ma vileji
hedemani) mchigaba chakhe vyakukhumbikwa
pakukapereka sembe ku Mbenji pakuwonga
kweneso kulomba mizimu kuti yipereke somba
zinandi nakuti ulovi uchitike kwambura ngozi.
Nga nthowa yimoza yakovwira pakulera
somba, Mbenji yikujarika ku nchito ya ulovi
kwambira mwezi wa December mpaka April na
chakulata chakupa mwabi somba kuti zibabane.
Pala pali mdauko wakujurira panji kujara ulovi,
Fumu Msosa yekha ndiyo yikulongozga midauko
iyi nangauli balalabalala baboma bakuchemeka
kwiza kaba nawo.
Ni Fumu Msosa yekha iyo yili na nkhongono
zakuzomerezga panji kukana fundo izo makomiti
ghakupambanapambana ghakwendeska nchito za
ulovi ku Mbenji ghangabika.
Balovi banandi bakuchimbizgika ku Mbenji
panji kubadara pala batondeka kulondezga
malango agho Fumu Msosa yabika.
Ndipo chifukwa chakuti somba zikufwa
zinandi kweneso ziweme, balovi bakuyezgeska
kupulikira malango agha n
Balimi bamvikaya bakusoba ulangizi
C
H
I
T
H
U
T
H
U
Z
I
:

N
A
T
I
O
N

L
I
B
R
A
R
Y
Malo ghaulovi
ghakumanyikwa
kuti ghakuba
pasi pa muuso
wa fumu
yakutiyakuti.
gha ulimi wa somba,
bayowoya ba Nyirenda.
Ba Nyirenda bati sukulu
iyi yili na basambizi 84.
Kwene bakughanaghana
v y a k u s a z g i r a p o s o
banyakhe 20.
Pala koleji iyi yamala,
Unilia yibenge na makoleji
yachitatu. Unilia yili na
sukulu ku Ekwendeni
mboma la Mzimba na ku
Livingstonia.
Pachisulu ku Ekwendeni,
sukulu iyi yikapereka ma
digili na ma dipuloma kwa
basambiri 165 abo bamala
masambiro ghabo.
Sukulu iyi yikamba mu
chilimika cha 2003 na
basambiri 500. Kwene
sono yikusambizga
banthu 1 000 chilimika
chilichose. n
Wupu wa abo
bakuguliska mbuto
wa Seed Traders
Association of Malawi
(Stam) walomba balimi
kuti bakhale maso na
mbuto izo bakugula
chifukwa pali banji abo
bakuguliska mbuto
zambura kuzomerezgeka
na boma.
Mlala wa Stam, ba
Dellings Phiri, bati
balimi bachenjere
chifukwa misika yinandi
mcharo chino yili na
mbuto izi.
Iwo bati pali chofyo
chakuti mbuto zambura
kuzomerezgeka izi
zingabika charo chino
paukavu chifukwa mbuto
zinandi mwa izi zikumera
chara.
Ba Phiri balombaso
makampani ghakuguliska
mbuto kuti ghamanye
vya ivi.
Makampani agha
ghasambizge balimi
vya mbuto zawo
mwakuti banthu baleke
kupusikika, bayowoya
ba Phiri.
Ba Phiri bati
Stam yabika banthu
bakhe mu misika
yakupambanapambana
mwakuti bakake munthu
waliyose wakuchita ivi.
Chenjerani na mbuto zambura kuzomerezgeka
Wupu wa balimi wa
Farmers Union of Malawi
(FUM) wazomerezga ivyo
Stam yasanga pa mbuto
zambura kuzomerezgeka
izi.
Mlala wa wupu uwu,
ba Alfred Banda, bati
FUM yasanga kuti banthu
banji bakuguliska mbuto
zambura kuzomerezgeka
pa misika ya mbuto za
sabuside.
Kwene mbuto za
banthu aba niziweme
chara chifukwa
zikusuzga pakumera.
Kwene mphakusuzga
kuti tibakole chifukwa
bakugwentha mnyengo
yene iyo baguliska mbuto
zawo, bati ntheura ba
Banda.
Iwo bati suzgo likulu
ndakuti malango gha
charo chino nganonono
chara pakumazga ivi.
Kwene muyowoyeri
wa unduna wa vyaulimi,
ba Sarah Tchowa, bati
boma lili na mbuto izo
lilikuzomerezga.
Ntheura, iwo balomba
makampani agho
ghalikuzomerezgeka
na boma kubika
vimanyikwiro vyawo
mwakuti balimi babe na
mwabi wakupambaniska
mbuto zakuzomerezgeka
na zambura
kuzomerezgeka.n
JOHN CHIRWA

You might also like